MAYANl BOYZ- DEDZA

MAYANl BOYZ- DEDZA

Share

History writer
Tech
& News by ki (KI) & MAYANI BOYZ, DEDZA DISTRICT
For booking 👉+27733691821

09/08/2026

wawat uko, tiyamike issue yatha tionane cha mma 1 muno

06/08/2026

MOYO PART 1

Linali mwezi wa Disembala. Mvula inali itayamba kale kugwa ku Lilongwe. M'misewu munali madambo ndi ana akusewera m'matope.

Ibrahim anali mnyamata wa zaka 19. Ankakhala ku Area 25 ndi azakhali ake. Makolo ake anamwalira onse pamene anali ndi zaka 12 chifukwa cha matenda. Kuyambira tsiku limenelo moyo unakhala wovuta.

Azakhali ake anali ndi ana atatu awo. Choncho chakudya m'nyumba munalibe nthawi zonse. Ibrahim ankadzuka 4 koloko m'mawa n'kunyamula katundu pa msika wa Lilongwe. Ankatulutsa matumba a ufa, shuga, ndi mpunga kwa amalonda. Pa tsiku anali kulandira 2000 kapena 3000. Ndalama imeneyo ankagula sopo, mchere, ndi chakudya cha tsikulo.

Tsiku limodzi kunali kotentha kwambiri. Ibrahim anamaliza ntchito nthawi ya 3 koloko masana. Thumba lomaliza lomwe ankatulutsa linali lolemera kwambiri. Pamene ankalinyamula, thumba linang'amba ndipo ufa wonse unathira pansi.

Mwini malonda anafuula. "Wachita chiyani iwe? Ufa uwu ndi 25,000! Ulipira!"

Ibrahim anagwada pansi n'kuyamba kutola ufa ndi manja onjenjemera. Misodzi inamuyandikira koma anayiluma. "Bwana ndikupepesa. Sindikudziwa. Ndidzagwira ntchito mpaka ndikulipira."

Mwini malondayo anamukankha. "Choka apa! Usabwerenso!"

Ibrahim anatenga chipewa chake chopanda kanthu n'kunyamuka. M'matumba mwake munali 500 yokha. Sanagule ngakhale buledi.

Anali kuyenda mwakachetechete pansi pa mvula yomwe inayamba kugwa pang'ono pang'ono. Anadutsa pa banki ina yaikulu. Kunja kwa bankiko kunali mayi wina atakhala pansi. Patsogolo pake panali thumba lalikulu lotseguka. Mkatimo munali mafayilo ndi ndalama za ku banki.

Mayiyo anali akulira. "Ah Mulungu wanga. Ndaiwala thumba langa mu taxi. Onse atenga ndalama za kampani."

Ibrahim anaimirira. Mtima wake unali kunena "tenga ndalamazo n'uthawa. Palibe amene akuwona." Koma phazi lake linayima.

Anapita kwa mayiyo. "Mayi musalire. Ndikuthandizani kunyamula."

Mayiyo anamuyang'ana ndi maso odzala misozi ndi mantha. "Ndalama izi ndi za kampani. Ngati zatayika nditha kuthamangitsidwa."

Ibrahim anathandiza mayiyo kunyamula thumba. Ndi manja ake adawerenga ndalama mwachangu. Munali pafupifupi 2 million.

Mayiyo anagwira dzanja la Ibrahim. "Zikomo mwana. Dzina lako ndi ndani?"

"Ibrahim. Ndikugwira ntchito kunyamula katundu pa msika."

"Waitira apa. Ndikubwerera." Mayiyo analowa mubankimo.

Mphindi 10 zitadutsa anatuluka ndi envelope. "Izi ndi zako. Ndalama ya kukhulupirika kwako. Ndipo ndikufuna ndikulembe ntchito ku kampani yathu."

Ibrahim anayang'ana envelope. Mkati mwake munali 50,000. Ndalama imene sanali atagwirapopo m'moyo wake wonse.

Anangoti ndi maloto.

PHUZILO LA PART 1
Kukhulupirika m'zing'ono kumakufikitsa ku zinthu zazikulu. Nthawi zina Mulungu amakuyesa ndi chinthu chaching'ono asanakupatse chachikulu...
Tikumanenso Ku part 2

Part 2 ili uku ?Mayani TC Dedza &
https://chat.whatsapp.com/Bo1A6gcI6nf8AI0LfLsm0l
Tapangan follow Mayani Boyz - Dedza

06/08/2026

🤵Koma akulu akulu, mkazi wanga ndiwanzelu, eti kumaweta mbuzi ine ndisakudziwa
👨‍👩‍👧‍👦Waziona Kuti ase,
🤵Mufon mwake dapeza message yoti, Kodi mbuzi yako ija ilipo?

😭😭😭😭 Koma ukaledzela Aish!!! Mavuto
Follow 👉 Mayani TC Dedza + Mayani Boyz - Dedza + Kusengwe Iwen +

06/08/2026

⚠️⚠️⚠️: kwa onse amene mmatsata khani zathu, page yathu yatenga issue kotelo khani zathu zonse, zizipezeka uku 👉 Mayani TC Dedza tapangani follow

06/08/2026

🚴... 🚶Man tatitengen
🚴........... 🚶Brow chonde
🚴................. 🏃Brow taiman
🚴...................... 🚶 Pathako pako
😂

05/08/2026

MILLIONAIRE BOY - PART 6 LAST

Chaka chimodzi chapita.

Chifundo tsopano anali ndi garage yake yaing'ono. Ankalikonza magalimoto ndi manja ake. Analibe miliyoni, koma anali ndi mtendere.
Angella anali atasamalira maphunziro ake. Analembetsa ku College of Nursing. Anali woyamba pa class.

Tsiku limenelo dzuwa linali lotentha koma lokongola.
Patsogolo pa tchalitchi ting'ono ku Area 18 panali anthu ochepa. Palibe Range Rover. Palibe suti zodula.
Panali Chifundo atavala suti yobwereka. Ndipo Angella atavala diresi yoyera yosavuta, koma ankawalira ngati mngelo.
Mwamuona Angella mmene wakongolera 😭

Pambali pake panali Amayi ake atakhala pa wheelchair, wathanzi. Ndipo Blessings atavala suti yaing'ono.
Kumbuyo kwa tchalitchi... panali Bambo Soko ndi Mai Soko. Chete. Akungoyang'ana.

Pastor anafunsa: "Ndani akupereka mtsikanayu?"
Bambo Soko ananyamuka pang'onopang'ono. Anayenda nkapita patsogolo.
"INE" anatero ndi liwu logwedezeka.
Anatenga dzanja la Angella nkuliyika m'dzanja la Chifundo.
"Ndanena zambiri zoyipa za iwe mwana wanga. Lero ndikukupepesa. Undiphunzitse chikondi chenicheni."

Mai Soko anabwera ndi maluwa. Anapereka kwa Angella.
"Takulandirani m'banja mwathu mwana wanga."

Chifundo ndi Angella anasinthana mphete. Zopangidwa ndi siliva chabe.
"Ndikulonjeza kukukonda, ngakhale tilibe kalikonse" Chifundo anatero.
"Ndipo ine ndikukuloonjeza kuyima pambali pako, ngakhale dziko lonse likhale lotsutsa" Angella anayankha.

Anthu onse anafuula: "M***a kumkiss mkwatibwi wanu!"

ZAKA 5 KUTSIKU LUMENEPO

Garage ya Chifundo inali itakula. Analinso ndi kampani yaing'ono ya ma transport.
Angella anali Nurse wamkulu kuchipatala. Amayi ake anali bwino. Blessings anali ku Secondary School.
Ndipo pa robot ya Area 3 pomwe Angella ankafuwula "ma orange"...
Panali bango lalikulu lolemba...

Tsiku lina mnyamata anafika ku garage.
"Uncle, ndingagwile ntchito pano? Amayi anga amagulitsa ma tomato."
Chifundo anayang'ana Angella. Anamwetulira.
"Ndiwe wotani?"
"Ndikufuna kukhala ngati inu bwana."

Chifundo anamugwira phewa. "Ndiye tiyeni tigwire ntchito mwana wanga."

MATHERO

Chifundo sanasankhe ndalama.
Anasankha chikondi.
Ndipo chikondi chimenecho chinamupatsa chilichonse.

MORAL Simufunika kukhala ndi miliyoni kuti ukhale ndi moyo wa miliyoni. Ufuna mtima umodzi woona

Zikomo powerenga nkhaniyi ❤️
Ngati yakukhudza share ndi anzako kuti nawonso amve.


Tapangan follow Mayani Boyz - Dedza
Tikumanenso ku S2/ season 2 + Khani Ina yatsopano
Mukafuna Ku WhatsApp group link
https://chat.whatsapp.com/Bo1A6gcI6nf8AI0LfLsm0l

05/08/2026

MILLIONAIRE BOY - PART 5

Nyumba ya a Soko. Chipinda cha msonkhano.
Patebulo panali Bambo Soko, Mai Soko, Tasila, Linda komanso amalume awiri a Chifundo.

Chitseko chinatseguka. Chifundo analowa. Wekha.
"Kodi Angella ali kuti?" Tasila anafunsa ndikuseka.
"Ali kunyumba kwake. Kumene kuli mtendere." Chifundo anayankha nkhani.

Bambo Soko anakwera magalasi ake.
"Mwana wanga, timakukonda. Koma chomwe ukuchitachi ndi manyazi kwa banja lathu. Ukudziwa kuti tikukonza ukwati wako ndi Natasha- mwana wa a Banda. Banja la miliyoni ngati lathu."
Mai Soko anawonjezera: "Natasha ali ndi digiri. Ali ndi nyumba. Ali ndi mbiri. Koma kagaluka ka ma orange..."

"Kulekani kumulankhula choncho!" Chifundo anafuula. Tebulo linagwedezeka.
"Angella amagwila ntchito kuposa inu nonse! Iye amadyetsa banja lake. Iye amasamalira amayi ake odwala. Koma inu? Mukukhala ndi ndalama za bambo zija."

Amalume mmodzi anaimirira. "Chifundo, ngati upitiliza ndi mtsikanayu, tidzakuchotsa ku ma company onse. Sipadzakhala galimoto, sipadzakhala nyumba, sipadzakhala ndalama."

Chipindacho chinakhala chete.
Chifundo anangomwetulira. Anatulutsa wallet yake. Anatulutsa ATM card nkuika pa tebulo.
"Ndibweze. Ndalama zanu. Nyumba yanu. Galimoto yanu."
Kenako anavula watch yake ya Rolex nkuika pamenepo.
"Koma simungathe kunditenga chinthu chimodzi. Mtima wanga."

Anayang'ana banja lake lonse m'maso.
"Ndasankha. Ndasankha Angella
Ngati ndinu banja langa, bwerani tikamudziwe. Ngati ayi... ndiye ndachita bwino kukhala ndi banja latsopano."

Anatembenuka natuluka. Palibe amene anamuletsa.

MAWA LAKE

Chifundo anabwera kunyumba kwa Angella ndi taxi. Palibe Range Rover.
Anali ndi thumba limodzi lokha.
Amayi a Angella ndi Blessings anadabwa.
"Mwana wanga, wachita chiyani?"
Chifundo anagwada. "Amayi, ndachoka kwao. Ndasankha Angella. Ndilibe ndalama tsopano. Koma ndili ndi manja awiri. Ndidzagwila ntchito."

Angella analira. "Chifundo... sungathe kuchita izi chifukwa cha ine..."
Chifundo anamukumbatira. "Nditha. Chifukwa ndiwe wofunika kuposa ma company onse a bambo."

Blessings anathamangira nati: "Ndiye tiyeni tigulitse ma orange limodzi Uncle Chifundo!"
Onse anaseka. Ngakhale anali ndi misozi.

Masabata awiri atapita...
Chifundo anayamba kugwila ntchito ku garage. Angella anayamba sukulu ya unamwino ndi ndalama zomwe Chifundo ankasunga.
Amayi a Angella anapeza mankhwala. Thanzi lake linayamba kuyenda bwino.

Tsiku lina, pa robot ya Area 3...
Galimoto ina inaimira. Inali Range Rover.
Watsika Bambo Soko yekha.
Anayang'ana Chifundo akunyamula tayala. Atavala ma overall odetsedwa.
Pambali pake panali Angella, atavala uniform ya kusukulu ya unamwino, akumuthandiza.

Bambo Soko anayandikira.
"Mwana wanga..."
Chifundo anaimirira. Anapukuta manja.
"Bambo."
"Ndabwera kukuuza kuti... ndanyadira nawe."..
Ikupitililabe ...

Tapangan follow?Mayani Boyz - Dedza kuzatela pamalo
Tapangan join group lathu la WhatsApp link
https://chat.whatsapp.com/Bo1A6gcI6nf8AI0LfLsm0l

03/08/2026

MILLIONAIRE BOY - PART 4

Galimoto ya Range Rover inaimira kutsogolo kwa nyumba yaing'ono ya njerwa ku Area 25.
Padenga panali ma sheet. Pakhomo panali nsalu yakale.

Angella anatsika pang'onopang'ono. Mtima wake unali ukumenya.
"Chifundo... nyumba yathu ndi yaing'ono... ukhoza kusekedwa..."
Chifundo anamuyang'ana nati: "Angella, nyumba siyimanga munthu. Munthu ndiye amamanga nyumba."

Anatenga masonga 5 a zovala nkulowa nawo.
Mkati munali Amayi a Angella atagona pa mat. Anali odwala. Pambali pake panali Mchimwene wake, Blessings wa zaka 12, akuphika nshima.

"Amayi..." Angella anayitana.
Amayi anadzuka. Atamuona Angella ndi diresi yoyera ndi masonga m'manja, anangodabwa.
"Mwana wanga? Izi zachokera kuti?"
Blessings anaponya supuni pansi. "Sis Angella? Ndi ndani uja?"

Panthawiyo Chifundo analowa. Wamtali, wovala suti.
Nyumba yaing'ono yonse inangodzaza.
"Good evening Amayi. Dzina langa ndine Chifundo Soko." anatero ndikugwada pansi ngati mwana wamwambo.

Amayi a Angella anangoyang'ana. Sananene kalikonse kwa kanthawi.
"Ndiye iwe ndiwe unampatsa mwana wanga zovala izi?"
"Inde Amayi. Koma si chifukwa chakuti ndine ndi ndalama. Ndi chifukwa chakuti ndikufuna kumusamalira Angella."

Blessings anathamangira kwa Angella. "Sis! Utipeze kuti ma orange?"
Angella anamukumbatira. Anayamba kulira. "Sitikufunikanso kugulitsa ma orange Blessings. Mulungu watiyankha."

Amayi anayang'ana Chifundo kuchokera kumutu mpaka ku phazi. Kenako anati:
"Mwana wanga. Ndalama zikatha, munthu amatsala. Ukufunadi mwana wanga?"
Chifundo anagwada patsogolo pa Amayi. "Amayi, ndikulonjeza. Ndidzamusamalira Angella ngati diso langa. Ndipo ndidzakuthandizani inunso ndi mankhwala anu."

Amayi anapumira kwambiri. Kenako anangomwetulira. Misozi inatuluka.
"Mulungu akudalitse mwana wanga. Angella wanga wazunzika kwambiri."

Panthawiyo foni ya Chifundo inali.
Ndi Bambo Soko
"Chifundo, bwerera kunyumba pompano. Tiyankhule. Kapena uyiwala kuti ndiwe mwana wanga."

Chifundo anayang'ana Angella. Anagwira dzanja lake.
"Amayi, ndiyenera kupita. Koma ndibwerera mawa. Ndi doctor. Ndi chakudya. Ndi chilichonse chimene mukusowa."

Anakiss Amayi m'manja. Anatenga Angella nathawa.

Atangotuluka, Blessings anati: "Amayi, kodi uyu ndi mchimwene wanga watsopano?"
Amayi anangomwetulira ndikuyang'ana padenga. "Mwina Mulungu wamva mapemphero athu mwana wanga."

Koma ku nyumba ya a Soko... msonkhano wabanja unali uyamba...
Ikupitililabe.

Tapangan follow
Mayani Boyz - Dedza

03/08/2026

MILLIONAIRE BOY - PART 3

Nyumba ya a Soko ku Area 10 inali yaikulu ngati hotel. Pali dziwe losambira, pali alonda pakhomo.
Galimoto ya Chifundo itangolowa, alonda anatsegula gate mwachangu.

Koma mkati mwa nyumba... mpweya unali wolemera.
Mai Soko anali atakhala pa sofa. Atavala diresi ya kutchova. Pambali pake panali Bambo Soko ndi alongo awiri a Chifundo - Tasila ndi Linda

Chifundo analowa. Kumbuyo kwake Angella Atavala diresi yoyera yochokera ku shopu. Atagwira masonga a zovala.

Nyumba yonse inakhala chete.
Tasila anaphimba pakamwa. Linda anangoyang'ana Angella kuchokera kumutu mpaka ku phazi nkusemula.

"Chifundo... uyu ndani?" Mai Soko anafunsa ndi liwu lozizira.
"Mama, uyu ndi Angella. Ndikufuna mumudziwe."
"Angella?" Bambo Soko anaseka mopanda chisangalalo. "Dzina la mtsikana wogulitsa ma orange pa robot?"

Angella anagwetsa mutu pansi. Manja ake anayamba kunjenjemera.
"Mukudziwa bwanji?" Chifundo anafunsa mokwiya.
"Tili ndi maso mwana wanga. Mzinda wonse ukulankhula za iwe ndi kachiswe ka m'msewu." Tasila anatero.

Mai Soko ananyamuka. Anayandikira Angella. Anamuyang'ana kuchokera kumutu mpaka ku phazi.
"Diresi yabwino. Koma imatha kubisa chiyani?"
"Mama lekani" Chifundo anafuula.
"Ayi ndisiye? Banja lathu lili ndi mbiri Chifundo! Sitingakwatire mtsikana wopanda makolo, wopanda maphunziro, wogulitsa ma orange!"

Angella misozi inayamba kutuluka.
"Zikomo chifukwa cha zovala bwana... koma ndikhoza kupita..." anatero ndi liwu lochepa.
"Ayi" Chifundo anagwira dzanja lake mwamphamvu. "Sukupita kulikonse."

Anayang'ana banja lake lonse m'maso.
"Mukundiseka chifukwa chakuti amayi ake amagulitsa ma orange? Koma ine ndili pano chifukwa chakuti bambo anga anali ndi ndalama! Kusiyana kwake ndi chiyani?"
"Chifundo..."
"Ayi! Lero ndaphunzira chinthu. Ndalama sizigula mtima wabwino. Angella amagwila ntchito kuti adyetse banja lake. Iye ndi wolimba kuposa aliyense pano!"

Anatembenukira kwa Angella. Anapukuta misozi yake ndi chala.
"Osalira. Kuyambira lero, iwe ndi ine. Ngati banja langa silikukufuna... tidzamanga banja lathu."

Anatenga masonga onse. Ndi dzanja limodzi anagwira Angella.
"Tikupita."

Atangotuluka pakhomo, Mai Soko anafuula: "Ukutuluka ndi iye, usabwerere kuno!"

Chifundo sanayang'ane kumbuyo.
Anamutsegulira Angella chitseko cha Range Rover.
"Angella, ukufuna kupita kuti? Kunyumba kwako?"
Angella anagwedeza mutu. "Inde... koma amayi anga ndi mchimwene wanga... adzadabwa kuona zovala zimenezi..."
Chifundo anamwetulira. "Ndiye tiwadabwitse pamodzi."
Ikupitililabe

Tapangan follow Mayani Boyz - Dedza
& Join group lathu la WhatsApp link
https://chat.whatsapp.com/Bo1A6gcI6nf8AI0LfLsm0l

02/08/2026

MILLIONAIRE BOY - PART 2

Range Rover inaimira patsogolo pa Shopu ya Antony
shopu yaikulu kwambiri ya zovala ku Lilongwe.
Anthu mkati mwa shopu anangodabwa kuona Chifundo alowa ndi mtsikana wovala diresi yong'ambika komanso nsapato za rabara.

"Chifundo mwana? Wakwera ndi ndani uja?" a cashier anafunsa mokweza.
Chifundo sanayankhe. Anagwira dzanja la Angella mwamphamvu.
"Good afternoon. Ndikufuna mutenge mtsikanayu mumpatse zovala zonse zabwino zomwe muli nazo. Kuchokera kumutu mpaka ku phazi."

Angella anagwedezeka. "Ayi bwana... ndili bwino chonchi..."
Chifundo anamuyang'ana m'maso nati mwakachetechete: "Angella, lero ndi tsiku lako. Lolani ndikuimilire. Palibe chifukwa chomvera manyazi."

Anamutenga nampita ku section ya madiresi.
"Yesani awa onse" anauza a shop attendant.
Angella analowa mu fitting room. Mtima wake unali ukumenya. Iye sanavalepo diresi yodula chonchi m'moyo wake.

Pakadali pano foni ya Chifundo inali.
Ndi Amayi ake - Mai Soko.
"Chifundo uli kuti? Ndawona pa status kuti uli ndi mtsikana wina? Wochokera kuti?"
"Mama tidzakambirana kunyumba. Koma ndikusangalala naye."
"Chifundo! Ukudziwa kuti banja lathu silikwatira anthu a m'msewu! Choka kwa iye tsopano!"

Chifundo anadula foni. Anapumira.

Pakadali pano Angella anatuluka.
Anali atavala diresi yoyera, yayitali, yokhala ndi maluwa ang'onoang'ono. Tsitsi lake anamukongoletsa.
Shopu yonse inakhala chete.

Mwamuona Angella mmene wakongolera.
Anali ngati mfumukazi. Ngakhale a shop attendant anangoti "wow".

Chifundo anangoyimirira. Sananene kalikonse kwa masekondi 10.
Kenako anati: "Tengani zovala zonse 10. Ndi nsapato, ndi bag, ndi zonunkhira. Chilichonse."

Anzake a Chifundo omwe anali kudikira kunja analowa.
"Wabwana iwe wasintha" mmodzi anatero. "Koma kodi banja lako lidzavomereza?"
Chifundo anayang'ana Angella nati: "Ine ndasankha. Ngati sakufuna, ndi vuto lawo."

Anatuluka ndi masonga 5 a zovala. Anamuika Angella mu galimoto.
Asananyamuke, Angella anati: "Zikomo Chifundo. Koma... bwanji ukundithandiza chonchi? Simundidziwa."
Chifundo anamwetulira nati: "Chifukwa ndikuona iwe. Osati zovala zako. Osati banja lako. Ndiwe Angella. Ndipo ndiwe wokwanira."

Galimoto inanyamuka. Koma kumbuyo kwawo...
Mai Soko anali atayima pakhomo la shopu. Ataona zonse. Ndipo nkhope yake inali yodzala ndi mkwiyo...
Ikupitililabe tapangan follow Mayani Boyz - Dedza + join group lathu la WhatsApp link
https://chat.whatsapp.com/Bo1A6gcI6nf8AI0LfLsm0l
Osaiwala share

Want your establishment to be the top-listed Arts & Entertainment in Dedza?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Website

Address

Mayani
Dedza

Opening Hours

Monday 07:00 - 20:30
Tuesday 07:00 - 20:30
Wednesday 07:00 - 20:30
Thursday 07:00 - 20:30
Saturday 06:00 - 12:30
Sunday 07:00 - 20:00